nyanja_reg/62-2PE.usfm

126 lines
8.5 KiB
Plaintext
Raw Permalink Normal View History

2021-10-05 20:11:56 +00:00
\id 2PE
\ide UTF-8
\h 2 Petulo
\toc1 2 Petulo
\toc2 2 Petulo
\toc3 2pe
\mt 2 Petulo
\s5
\c 1
\cl Mutu 1
\p
\v 1 Simon Petulo, kapolo ni mpositoli wa Yesu Khristu kwa onse bamene banalandira chikhulupiliro cholingana na chamene talandira, chikhulupiliro na kuyera kwa mulungu na mpulumusi wathu Yesu Khristu.
\v 2 Lekani cisomo na mtendere zinkhale zambiri pa zinthu za Mulungu na Yesu Khristu ambuye athu.
\s5
\v 3 Zinthu zonse za mphamvu ya moyo na umulungu zinapasidwa kwa ife pa kuziba Mulungu amene anatiitana mwa mphamvu zake.
\v 4 Kupitira mwa izi anatipasa malonjezo yambiri yakulu kuti munkhale otengako mbali pa zinthu zabwino, kuti musapezeke mu mabvuto yomwe yali mu ziko chifukwa cha kuzikonda.
\s5
\v 5 Pa ichi, muyeseko kubweresa mtendere chifukwa cha chikhulupiriro chanu, ubwino wanu kamba ka zamene muziba za Mulungu.
\v 6 Pa kuziba kwanu, mufakepo kuzilesa elo pa kuzilesa kwanu mufakepo kukosa elo pa kukosa kwanu mufakepo kuziba Mulungu.
\v 7 Pa kuziba Mulungu kwanu mufakepo kukonda ba bululu banu elo pa kukonda banzanu mufakepo chikondi.
\s5
\v 8 Ngati izi zonse zili mwa inu elo zikula mkati kanu, simuzakangiwa kubala zipaso pa zamene muziba za ambuye Yesu Khristu.
\v 9 Koma aliyense amene alibe izi zinthu amaona zamene zili pafupi chabe; alibe menso. Aibala kusukidwa ku machimo yake yakudala.
\s5
\v 10 Manje, ba bululu, muyenera kuyesa kuchita zamushe kuti kuitanidwa na kusankidwa kwanu kusankhale kobvuta. Ngati mwachita izi zinthu, simuzagwa.
\v 11 Ngati mwachita zimenezo ndiye kuti ufumu wa kumwamba wa ambuye Yesu Khristu uzapasidwa kwa inu.
\s5
\v 12 Kotero ine nizankhala okonzeka kukukumbusani pa izi zinthu nangu kuti muviziba kudala, nangu kuti munakosa kudala mu chikhulupiliro manje.
\v 13 Niona ni chinthu chabwino kukukumbusani na kukupasani mphamvu pa izi malinga ngati nili mu tenti.
\v 14 chifukwa niziba ati manje-manje nizachosa tenti, monga mwamene Yesu Khristu anionesera.
\v 15 Nizayesesa kuti mukazikumbuka izi zinthu pamene ine nizayenda.
\s5
\v 16 Chifukwa sitinakonkhe maningi zinthu za boza zamene zinapangidwa pamene tinamuuzani za mphamvu na kuonekera kwa ambuye athu Yesu Khristu. koma tenzeli mboni ya ukulu wake.
\v 17 Chifukwa analandira kwa Mulungu atate ulemu na ulemelero pamene mau yanaletewa kwa yeve na mphamvu za Mulungu kukamba ati, "uyu ni mwana wanga, okondewa wanga, wamene nikondwera nayeve."
\v 18 Tinamvera mau aya yamene yanachoka kumwamba, pamene tinali nayeve pa lupiri loyera.
\s5
\v 19 Tili na mau aya ya uneneri yosimikizirika. Muzachita mushe ngati mwamvera. Ili ngati nyale yowala younika mu m'dima kufika kuseni na nyenyezi ituluka mu mitima yanu.
\v 20 Muzibe ichi poyamba, ati palibe uneneri wamene uli na kutantauzila kwa kaena.
\v 21 palibe uneneri wamene umabwera pa chifuniro cha munthu. Koma banthu bamene banatengewa na mzimu oyera banamvera kwa Mulungu.
\s5
\c 2
\cl Mutu 2
\p
\v 1 Aneneri aboza anabwera kwa anthu, naonso aphunzisi aboza azabwera kwa inu. Azaleta zipunziso zaboza, elo bazakana mukulu amene anabagula. Baziletela mabvuto pali beve beka.
\v 2 Banthu bambiri bazabakonkha, elo chifukwa cha beve chilungamo chizaonongeka.
\v 3 Chifukwa cha kuzikonda bazapangirapo pindu pali imwe chifukwa cha mau yao yaboza. Chiweruzo chao chizabwera manje-manje; kuonongeka kwao sikugona.
\s5
\v 4 Chifukwa Mulungu sanaleke angelo bamene banachimwa. Anabapereka kwa Tartarus kuti bankhale mu cheni ya kumidima mpaka pa nthawi ya chiweruzo. komanso, sanalekelele dziko la kudala.
\v 5 mu malo mwake anasunga Noah wamene anali oyera mtima, pamozi na benangu asanu ndi awiri, pamene analeta mvula yosasila pa dziko la banthu ochimwa.
\v 6 Mulungu anaonongaso Sodom na gomorrah na moto, ngati chisanzo cha chilango chamene chizabwera kusogolo.
\s5
\v 7 Koma Lot oyera, amene enze anankhala pakati pa banthu ochimwa, Mulungu anamupulumusa.
\v 8 Kwa uja munthu osachimwa, amene enze kunkhala pakati pao masiku onse, enzeli kubvutika mu mtima pa zimene anali kuona na kumvera.
\v 9 Mulungu amaziba mopulumusila anthu ake kuchoka mu mayesero, na kuziba motengera banthu oipa kuti balandire chilango pa siku la chiweruzo.
\s5
\v 10 Izi zinkhala zoona kwa baja bamene bapitirira kuchita zinthu zoipa kulingana na zamene thupi lao lifuna nakukana kumvera lamulo. Ndi olimba mtima komanso odzala ni chifuniro. Sayopa kunyoza banthu ozozedwa.
\v 11 Angelo ali ndi mphamvu zambiri, koma sabweresa manyozo ya chiweruzo pa iwo kwa ambuye.
\s5
\v 12 Koma izi nyama zopanda nzeru zinapangiwa kuti zigwidwe mu chionongeko. Saziba chamene atukwana. Muchionongeko
\v 13 bazapeza mpaso ya machimo ao. Aona monga kusangalala kwa masana nikwabwino. ni odesedwa na zoipa. Amamva bwino akamachita zinthu zao zoipa pomwe alikudya nanu.
\v 14 Ali na menso yozula na bakazi ba chiwelewele; sakhutira nao machimo. Amatuntha mitima yofoka kuti yachite zoipa, ndipo mitima yao yanaphunzisidwa kukhumbwa vinthu. Ni bana ba tembelero.
\s5
\v 15 Ataya njira yabwino. Anasokera, nasata njira ya Balaam mwana wa Boer, omwe akonda kulandira malipiro ya machimo.
\v 16 Koma analandira chizuzulo pa zoipa zake. Bulu osakamba koma kukamba mau ya munthu analetsa utsiru wa mneneri.
\s5
\v 17 Anthuwa ali ngati nyenje yopanda madzi. Ali ngati mmakumbi yamene mphepo imayendesa. Mdima olema unasungiwa pali beve.
\v 18 Bakamba na nthota zopanda pindu. Bamanyengelera banthu na zofuna za thupi lao. Bamanyengelera banthu bamene bafuna kuthaba bamene bankhala mu zoipa.
\v 19 Bamalonjeza mutendere kwa beve, koma beve nibakapolo ba zoipa. Chifukwa munthu nikapolo wa vamene vimubvuta.
\s5
\v 20 Aliyense wamene apewa chionongeko cha dziko lapansi kusebenzesa chizibiso cha Yesu Ambuye wathu, koma abweleranso ku zoipa, ndiye kuti chothera chinkhala choipa maningi kuchira choyamba.
\v 21 Chinakankhala bwino kuti sibanazibe zabwino kuchira kuziba na kubwelera futi ku zoipa kusiya malamulo yamene yenze banapasiwa.
\v 22 Mwambi uyu niwazoona pa beve: " galu abwelera futi ku vamene waluka. Nkhumba yosambika bwino imabwelera futi ku matika."
\s5
\c 3
\cl Mutu 3
\p
\v 1 Manje, nilemba kwa inu, okondewa, nkhalata iyi ya chiwiri ngati chikumbuso cha ku maganizo yanu,
\v 2 kuti mukumbukire zamene zinakambika kudala naba neneri oyera na lamulo la ambuye Yesu Khristu kupasiwa naba positoli banu.
\s5
\v 3 Ziwani izi poyamba, kuti banthu bovuta bazabwera mu masiku yosiliza. Bazakamba voipa na kupitirira kuchita zofuna zao.
\v 4 Bazakamba, " ili kuti lonjezo ya kubweraso kwake? kuchoka pamene batate bathu banagona zinthu zonse zili chimozi-mozi, kuchoka pamene chalo chinapangiwa."
\s5
\v 5 Baibalira dala kuti kumwamba na dziko la pansi zinapangiwa kuchoka ku manzi na manzi, kudala kulingana na malamulo ya Mulungu.
\v 6 Nakuti chifukwa cha izi zinthu, dziko la kudala linaonongewa, kuzula na manzi.
\v 7 Koma manje dziko liyembekeza chiweruzo cha muliro kulingana na lamulo limozi-mozi. Bachisungira siku la chiweruzo na kuonongeka kwa banthu ochimwa.
\s5
\v 8 Simuyenera kuibala, okondewa, kuti siku limozi kwa Mulungu ili ngati zaka 1000, elo zaka 1000 zili ngati siku imozi kwa Mulungu.
\v 9 Mulungu samachedwa pa malonjezo yake, monga mwamene benangu bangaonere kuchedwa. M'malo mwake niodekha mtima pa inu. Safuna ati umozi wa inu akaonongeke, koma aliyense apange malo ya kuleka zoipa.
\s5
\v 10 Koma, siku la ambuye lizabwera monga kawalala: Dziko lizatha na chongo chachikulu. Zinthu zizapsya na muliro, ndipo dziko na nchito zonse za mkati zizaziwika.
\s5
\v 11 Pakuti zinthu zonse zizasila motere, inu muzankhala banthu ba bwanji? Mufunika kunkhala umoyo wabwino wa umulungu.
\v 12 Mufunika kuyembekeza kubwera kwa siku la Mulungu. Pa siku limenelo, miyamba izaonongewa na muliro, na zonse zizasungunuka kamba ka kupya.
\v 13 Koma kulingana na malonjezo yake, tikali kuyembekeza kumwamba kwasopano na dziko lasopano, mwamene banthu babwino bazankhala.
\s5
\v 14 Kotero, okondewa, pakuti muyembekeza izi zinthu, muchite zonse zamene mungakwanise kuti mukapezeke mulibe bvuto pa menso pa Mulungu, muli yeve.
\v 15 Komanso muone kuchedwa kwa ambuye kunkhala ngati kudekha mtima kwake kukhala cipulumus o, monga momwe m'bale wathu Paulo analembera inu, kulingana na nzeru zamene zinapasidwa kwa yeve.
\v 16 Paulo akamba pa izi zinthu mu makalata yake yonse, mwamene muli zinthu zobvuta kumvesesa. Mbuli na banthu osankhazikika bamasokoneza zinthu zimenezi, mwamene bamachitira malemba yenangu, kuti bakaonongedwe.
\s5
\v 17 Kotero, okondewa, pakuti muziba izi zinthu, muzichinjirize kuti musasokonezewe na chinyengo cha anthu oipa ndi kutaya chilungamo chanu.
\v 18 Koma kulani mu cisomo ndi nzeru za ambuye ndi mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Ulemelero unkhale kwa yebve lero na nthawi zonse. Amen!